Kusabereka ndi chifukwa chosowa zipatso zenizeni mu mpingo wachiKhristu wamakono. Pali ntchito zambiri komanso mapulogalamu ambiri koma pali zipatso zochepa kapena palibe. Pali zambiri ku utumiki kuposa kupeza ziphaso zambiri za chidziwitso cha Baibulo. Abusa ambiri amagwa mu ulendo wawo chifukwa chokhumudwa komanso kunyengedwa chifukwa chakuti ndi osabala mu utumiki. Mulungu amafuna kuti tizibala zipatso. Mulungu akufuna kuti tiwonjezekere mu utumiki. Kuti mubereke muyenera kumvetsetsa kuti kusabereka kumatanthauza chiyani. Kusabereka ndi vuto lomwe Mulungu akufuna kuthana nalo mu utumiki wanu. Bukhu lapanthawi yake limeneli, lolembedwa ndi Dag Heward-Mills lidzakuthandizani kuleka kusabereka mu utumiki wanu. Mzimu wosabereka ukachotsedwa mudzayamba kubala zipatso. Mukutuluka mu kusabereka lero!